1 Wodala yense wakuopa Yehova, Wakuyenda m'njira zace.
2 Pakuti udzadya za nchito ya manja ako;Wodala iwe, ndipo kudzakukomera.
3 Mkazi wako adzanga mpesa wopatsa m'mbali za nyumba yako;Ana ako adzanga timitengo ta azitona pozinga podyera pako.
4 Taonani, m'mwemo adzadalitsikaMunthu wakuopa Yehova.
5 Yehova adzakudalitsa ali m'ZiyoniNdipo udzaona zokoma za Yerusalemu masiku onse a moyo wako.