1 M'mozamamo ndinakupfuulirani, Yehova.
2 Ambuye, imvani liu langa;Makutu anu akhale cimverereMau a kupemba kwanga.
3 Mukasunga mphulupulu, Yehova,Adzakhala ciriri ndani, Ambuye?
4 Koma kwa Inu kuli cikhululukiro,Kuti akuopeni.
5 Ndilindira Yehova, moyo wanga ulindira,Ndiyembekeza mau ace.
6 Moyo wanga uyang'anira Ambuye,Koposa alonda matanda kuca;Inde koposa alonda matanda kuca.
7 Israyeli, uyembekezere Yehova;Cifukwa kwa Yehova kuli cifundo,Kwaonso kucurukira ciombolo.