5 Ndilindira Yehova, moyo wanga ulindira,Ndiyembekeza mau ace.
6 Moyo wanga uyang'anira Ambuye,Koposa alonda matanda kuca;Inde koposa alonda matanda kuca.
7 Israyeli, uyembekezere Yehova;Cifukwa kwa Yehova kuli cifundo,Kwaonso kucurukira ciombolo.
8 Ndipo adzaombola IsrayeliKu mphulupulu zace zonse.