1 Yehova, kumbukilani Davide Kuzunzika kwace konse;
2 Kuti analumbira Yehova,Nawindira Wamphamvuyo wa Yakobo, ndi kuti,
3 Ngati ndidzalowa pakhomo pa nyumba yanga,Ngati ndidzakwera pa kama logonapo;
4 Ngati ndidzalola maso anga agone,Kapena zikope zanga ziodzere;
5 Kufikira nditapezera Yehova malo,Cokhalamo Wamphamvuyo wa Yakobo?