4 Ngati ndidzalola maso anga agone,Kapena zikope zanga ziodzere;
5 Kufikira nditapezera Yehova malo,Cokhalamo Wamphamvuyo wa Yakobo?
6 Taonani, tinacimva m'Efrata;Tinacipeza ku cidikha ca kunkhalango.
7 Tidzalowa mokhalamo Iye;Tidzagwadira ku mpando wa mapazi ace.
8 Ukani, Yehova, lowani ku mpumulo wanu;Inu ndi hema wa mphamvu yanu,
9 Ansembe anu abvale cilungamo;Ndi okondedwa anu apfuule mokondwera.
10 Cifukwa ca Davide mtumiki wanuMusabweze nkhope ya wodzozedwa wanu.