5 Kufikira nditapezera Yehova malo,Cokhalamo Wamphamvuyo wa Yakobo?
6 Taonani, tinacimva m'Efrata;Tinacipeza ku cidikha ca kunkhalango.
7 Tidzalowa mokhalamo Iye;Tidzagwadira ku mpando wa mapazi ace.
8 Ukani, Yehova, lowani ku mpumulo wanu;Inu ndi hema wa mphamvu yanu,
9 Ansembe anu abvale cilungamo;Ndi okondedwa anu apfuule mokondwera.
10 Cifukwa ca Davide mtumiki wanuMusabweze nkhope ya wodzozedwa wanu.
11 Yehova analumbira Davide zoona;Sadzalibweza; ndi kuti,Wa iwo okhala zipatso za thupi lako ndidzaika pa mpando wacifumu wako.