4 Tidati, Tidzayimba bwanji nyimbo ya YehovaM'dziko lacilendo?
5 Ndikakuiwalani, Yerusalemu,Dzanja lamanja langa liiwale luso lace.
6 Lilime langa limamatike ku nsaya zanga,Ndikapanda kukumbukila inu;Ndikapanda kusankha YerusalemuKoposa cimwemwe canga copambana.
7 Yehova, kumbukilani ana a EdomuTsiku la Yerusalemu;Amene adati, Gamulani, gamulani,Kufikira maziko ace.
8 Mwana wamkazi wa ku Babulo, iwe amene udzapasulidwa;Wodala iye amene adzakubwezera cilangoMonga umo unaticitira ife.
9 Wodala iye amene adzagwira makanda ako,Ndi kuwaphwanya pathanthwe.