1 Waucitsiru amati mumtima mwace, Kulibe Mulungu.Acita zobvunda, acita nchito zonyansa;Kulibe wakucita bwino.
2 Yehova m'Mwamba anaweramira pa ana a anthu,Kuti aone ngati aliko wanzeru,Wakufuna Mulungu.
3 Anapatuka onse; pamodzi anabvunda mtima;Palibe wakucita bwino ndi mmodzi yense.
4 Kodi onse ocita zopanda pace sadziwa kanthu?Pakudya anthu anga monga akudya mkate,Ndipo saitana pa Yehova.