4 Kodi onse ocita zopanda pace sadziwa kanthu?Pakudya anthu anga monga akudya mkate,Ndipo saitana pa Yehova.
5 Pamenepa anaopa-opatu:Pakuti Mulungu ali mu mbadwo wa wolungama.
6 Munyazitsa uphungu wa wozunzika,Koma Yehova ndiye pothawira pace.
7 Mwenzi cipulumutso ca Israyeli citacokera ku Ziyoni!Pakubweretsa Yehova anthu ace a m'nsinga,Pamenepo adzakondwera Yakobo, nadzasekera Israyeli.