8 Yehova, musampatse woipa zokhumba iye;Musamthandize zodzipanga zace; angadzikuze.
9 Kunena za mutu wao wa iwo akundizinga,Coipa ca milomo yao ciwaphimbe.
10 Makala amoto awagwere;Aponyedwe kumoto;M'maenje ozama, kuti asaukenso.
11 Munthu wamlomo sadzakhazikika pa dziko lapansi;Coipa cidzamsaka munthu waciwawa kuti cimgwetse.
12 Ndidziwa kuti Yehova adzanenera wozunzika mlandu,Ndi kuweruzira aumphawi,
13 Indedi, olungama adzayamika dzina lanu;Oongoka mtima adzakhala pamaso panu,