1 Yehova, ndaitana kwa Inu; ndifulumireni ine;Mundicherere khutu, pamene ndiitana kwa Inu.
2 Pempherolanga liikike ngaticofukiza pamaso panu;Kukweza manja anga kuikike ngati nsembe ya madzulo.
3 Muike mdindo pakamwa panga, Yehova;Sungani pakhomo pa milomo yanga.
4 Mtima wanga usalinge ku cinthu coipa,Kucita nchito zoipaNdi anthu akucita zopanda pace;Ndipo ndisadye zankhuli zao.
5 Akandipanda munthu wolungama ndidzati ncifundo:Akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu;Mutu wanga usakane:Pakuti pangakhale posautsidwa iwo ndidzawapempherera.
6 Oweruza ao anagwetseka pambali pa thanthwe;Nadzamva mau anga kuti ndiwo okondweretsa.
7 Mafupa athu amwazika pakamwa pa manda,Monga ngati akumba nanyimphula nthaka yapansi.