5 Akandipanda munthu wolungama ndidzati ncifundo:Akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu;Mutu wanga usakane:Pakuti pangakhale posautsidwa iwo ndidzawapempherera.
6 Oweruza ao anagwetseka pambali pa thanthwe;Nadzamva mau anga kuti ndiwo okondweretsa.
7 Mafupa athu amwazika pakamwa pa manda,Monga ngati akumba nanyimphula nthaka yapansi.
8 Pakuti maso anga apenya kwanu, Yehova Ambuye;Ndithawira kwa Inu; musataye moyowanga.
9 Mundisunge ndisagwe mumsampha anandicherawo,Ndisakodwe m'makwekwe a iwo ocita zopanda pace,
10 Oipa agwe pamodzi m'maukonde ao,Kufikira nditapitirira ine.