4 Potero mzimu wanga wakomoka mwa ine;Mtima wanga utenga nkhawa m'kati mwanga,
5 Ndikumbukila masiku a kale lomwe;Zija mudazicita ndilingirirapo;Ndikamba pa ndekha za nchito ya manja anu.
6 Nditambalitsira manja anga kwa Inu:Moyo wanga ulira Inu monga dziko lolira mvula.
7 Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha.Musandibisire nkhope yanu;Ndingafanane nao akutsikira kudzenje.
8 Mundimvetse cifundo canu mamawa;Popeza ndikhulupirira Inu:Mundidziwitse njira ndiyendemo;Popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu.
9 Mundilanditse kwa adani anga, Yehova;Ndibisala mwa Inu.
10 Mundiphunzitse cokonda Inu; popeza Inu ndinu Mulungu wanga;Mzimu wanu ndi wokoma; munditsogolere kucidikha.