1 Haleluya;Pakuti kuyimbira zomlemekeza Mulungu wathu nkokoma;Pakuti cikondwetsa ici, cilemekezo ciyenera.
2 Yehova amanga Yerusalemu;Asokolotsa otayika a Israyeli.
3 Aciritsa osweka mtima,Namanga mabala ao.
4 Awerenga nyenyezi momwe ziri;Azicha maina zonsezi.