1 Haleluya;Pakuti kuyimbira zomlemekeza Mulungu wathu nkokoma;Pakuti cikondwetsa ici, cilemekezo ciyenera.
2 Yehova amanga Yerusalemu;Asokolotsa otayika a Israyeli.
3 Aciritsa osweka mtima,Namanga mabala ao.
4 Awerenga nyenyezi momwe ziri;Azicha maina zonsezi.
5 Ambuye wathu ndi wamkuru ndi wa mphamvu zambiri;Nzeru yace njosatha.
6 Yehova agwiriziza ofatsa;Atsitsira oipa pansi.