11 Yehova akondwera nao akumuopa Iye,Iwo akuyembekeza cifundo cace.
12 Yerusalemu, lemekezani Yehova;Ziyoni, lemekezani Mulungu wanu.
13 Popeza analimbitsa mipiringidzo ya zitseko zanu:Anadalitsa ana anu m'kati mwanu.
14 Ndiyeamene akhalitsamalireanu mumtendere;Akukhutitsani ndi tirigu wakuca bwino.
15 Atumiza lamulo lace ku dziko lapansi;Mau ace athamanga liwiro.
16 Apatsa cipale cofewa ngati ubweya;Awaza cisanu ngati phulusa.
17 Aponya matalala ace ngati zidutsu:Adzaima ndani pa kuzizira kwace?