16 Apatsa cipale cofewa ngati ubweya;Awaza cisanu ngati phulusa.
17 Aponya matalala ace ngati zidutsu:Adzaima ndani pa kuzizira kwace?
18 Atumiza mau ace nazisungunula;Aombetsa mphepo yace, ayenda madzi ace.
19 Aonetsa mau ace kwa Yakobo;Malemba ace, ndi maweruzo ace kwa Israyeli.
20 Sanatero nao anthu amtundu wina;Ndipo za maweruzo ace, sanawadziwa.Haleluya.