2 Yehova amanga Yerusalemu;Asokolotsa otayika a Israyeli.
3 Aciritsa osweka mtima,Namanga mabala ao.
4 Awerenga nyenyezi momwe ziri;Azicha maina zonsezi.
5 Ambuye wathu ndi wamkuru ndi wa mphamvu zambiri;Nzeru yace njosatha.
6 Yehova agwiriziza ofatsa;Atsitsira oipa pansi.
7 Yamikani Yehova ndi kuthira mang'ombe;Myimbireni Mulungu wathu zamlemekeza pazeze:
8 Amene aphimba thambo ndi mitambo,Amene akonzera mvula nthaka,Amene aphukitsa msipu pamapiri.