8 Amene aphimba thambo ndi mitambo,Amene akonzera mvula nthaka,Amene aphukitsa msipu pamapiri.
9 Amene apatsa zoweta cakudya cao,Ana a khungubwi alikulira.
10 Mphamvu ya kavalo siimkonda:Sakondwera nayo miyendo ya munthu.
11 Yehova akondwera nao akumuopa Iye,Iwo akuyembekeza cifundo cace.
12 Yerusalemu, lemekezani Yehova;Ziyoni, lemekezani Mulungu wanu.
13 Popeza analimbitsa mipiringidzo ya zitseko zanu:Anadalitsa ana anu m'kati mwanu.
14 Ndiyeamene akhalitsamalireanu mumtendere;Akukhutitsani ndi tirigu wakuca bwino.