1 Haleluya.Lemekezani Yehova kocokera kumwamba;Mlemekezeni m'misanje.
2 Mlemekezeni, angelo ace onse;Mlemekezeni, makamu ace onse.
3 Mlemekezeni, dzuwa ndi mwezi;Mlemekezeni, nyenyezi zonse zaunikira.
4 Mlemekezeni, m'mwambamwamba,Ndi madzi inu, a pamwamba pa thambo.
5 Alemekeze dzina la Yehova;Popeza analamulira, ndipo zinalengedwa.
6 Anazikhazikanso ku nthawi za nthawi;Anazipatsa cilamulo cosatumphika.
7 Lemekezani Yehova kocokera ku dziko lapansi,Zinsomba inu, ndi malo ozama onse;