5 Alemekeze dzina la Yehova;Popeza analamulira, ndipo zinalengedwa.
6 Anazikhazikanso ku nthawi za nthawi;Anazipatsa cilamulo cosatumphika.
7 Lemekezani Yehova kocokera ku dziko lapansi,Zinsomba inu, ndi malo ozama onse;
8 Moto ndi matalala, cipale cofewa ndi nkhungu;Mphepo ya namondwe, yakucita mau ace;
9 Mapiri ndi zitunda zonse;Mitengo yazipatso ndi yamikungudza yonse:
10 Nyama za kuthengo ndi zoweta zonse;Zokwawa, ndi mbalame zakuuluka;
11 Mafumu a padziko ndi mitundu yonse ya anthu;Zinduna ndi oweruza onse a padziko;