1 Haleluya,Myimbireni Yehova nyimbo yatsopano,Ndi cilemekezo cace mu msonkhano wa okondedwa ace.
2 Akondwere Israyeli mwa Iye amene anamlenga;Ana a Ziyoni asekere mwa Mfumu yao.
3 Alemekeze dzina lace ndi kuthira mang'ombe;Amyimbire zomlemekeza ndi lingaka ndi zeze.
4 Popeza Yehova akondwera nao anthu ace;Adzakometsa ofatsa ndi cipulumutso,
5 Okondedwa ace atumphe mokondwera m'ulemu:Apfuule mokondwera pamakama pao,
6 Nyimbo zakukweza Mulungu zikhale pakamwa pao,Ndi lupanga lakuthwa konse konse m'dzanja lao;
7 Kubwezera cilango akunja,Ndi kulanga mitundu ya anthu;