1 Yehova, ndani adzagonera m'cihema mwanu?Adzagonera ndani m'phiri lanu lopatulika?
2 Iye wakuyendayo mokwanira, nacita cilungamo,Nanena zoonadi mumtima mwace.
3 Amene sasinjirira ndi lilime lace,Sacitira mnzace coipa,Ndipo satola msece pa mnansi wace.
4 M'maso mwace munthu woonongeka anyozeka;Koma awacitira ulemu akuopa Yehova.Atalumbira kwa tsoka lace, sasintha ai.