4 Zidzacuruka zisoni zao za iwo otsata mulungu wina:Sindidzathira nsembe zao zamwazi,Ndipo sindidzachula maina ao pakamwa panga,
5 Yehova ndiye gawo la colowa canga ndi cikho canga:Ndinu wondigwirira colandira canga,
6 Zingwe zandigwera mondikondweretsa;Inde cosiyira cokoma ndiri naco.
7 Ndidzadalitsa Yehova, amene anandicitira uphungu:Usikunso imso zanga zindilangiza.
8 Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse:Popeza ali pa dzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.
9 Cifukwa cace wasekera mtima wanga, nukondwera ulemu wanga;Mnofu wanganso udzakhala mokhazikika.
10 Pakuti simudzasiya moyo wanga kumanda;Simudzalola wokondedwa wanu abvunde.