1 Yehova, imvani cilungamo, mverani mpfuu wanga;Cherani khutu ku pemphero langa losaturuka m'milomo ya cinyengo,
2 Pankhope panu paturuke ciweruzo canga;Maso anu apenyerere zolunjika,
3 Mwayesera mtima wanga; mwandizonda usiku;Mwandisuntha, simupeza kanthu;Ndatsimikiza mtima kuti m'kamwa mwanga simudzalakwa.
4 Za macitidwe a anthu, ndaceniera ndi mau a milomo yanuNdingalowe njira za woononga.
5 M'mayendedwe anga ndasunga mabande anu,Mapazi anga sanaterereka.