4 Za macitidwe a anthu, ndaceniera ndi mau a milomo yanuNdingalowe njira za woononga.
5 M'mayendedwe anga ndasunga mabande anu,Mapazi anga sanaterereka.
6 Ine ndinakuitanani, pakuti mudzandiyankha, Mulungu:Cherani khutu lanu kwa ine, imvani mau anga.
7 Onetsani cifundo canu codabwiza, Inu wakupulumutsa okhulupirira InuKwa iwo akuwaukira ndi dzanja lanu lamanja.
8 Ndisungeni monga kamwana ka m'diso,Ndifungatireni mu mthunzi wa mapiko anu,
9 Kundilanditsa kwa oipa amene andipasula,Adani a pa moyo wanga amene andizinga.
10 Mafuta ao awatsekereza;M'kamwa mwao alankhula modzikuza.