10 Ndizo zifunika koposa golidi, inde, golidi wambiri woyengetsa:Zizuna koposa uci ndi zakukha za zisa zace,
11 Ndiponso kapolo wanu acenjezedwa nazo:M'kuzisunga izo muli mphotho yaikuru.
12 Adziwitsa zolowereza zace ndani?Mundimasule kwa zolakwa zobisika.
13 Ndiponso muletse kapolo wanu pa zodzitama;Zisacite ufumu pa ine: pamenepo ndidzakhala wangwiro,Ndi wosacimwa colakwa cacikuru.
14 Mau a m'kamwa mwanga ndi maganizo a m'mtima wanga abvomerezeke pamaso panu,Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga,