4 Muyeso wao wapitirira pa dziko lonse lapansi,Ndipo mau ao ku malekezero a m'dziko muli anthu.Iye anaika hema la dzuwa m'menemo,
5 Ndipo liri ngati mkwati wakuturuka m'cipinda mwace,Likondwera ngati ciphona kuthamanga m'njira.
6 Kuturuka kwace lituruka kolekezera thambo,Ndipo kuzungulira kwace lifikira ku malekezero ace:Ndipo kulibe kanthu kobisalira kutentha kwace.
7 Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo;Mboni za Yehova ziri zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru;
8 Malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima:Malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso.
9 Kuopa Yehova kuli mbe, kwakukhalabe nthawi zonse:Maweruzo a Yehova ali oona, alungama konse konse.
10 Ndizo zifunika koposa golidi, inde, golidi wambiri woyengetsa:Zizuna koposa uci ndi zakukha za zisa zace,