7 Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo;Mboni za Yehova ziri zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru;
8 Malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima:Malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso.
9 Kuopa Yehova kuli mbe, kwakukhalabe nthawi zonse:Maweruzo a Yehova ali oona, alungama konse konse.
10 Ndizo zifunika koposa golidi, inde, golidi wambiri woyengetsa:Zizuna koposa uci ndi zakukha za zisa zace,
11 Ndiponso kapolo wanu acenjezedwa nazo:M'kuzisunga izo muli mphotho yaikuru.
12 Adziwitsa zolowereza zace ndani?Mundimasule kwa zolakwa zobisika.
13 Ndiponso muletse kapolo wanu pa zodzitama;Zisacite ufumu pa ine: pamenepo ndidzakhala wangwiro,Ndi wosacimwa colakwa cacikuru.