1 Aphokoseranji amitundu.Nalingiriranji anthu zopanda pace?
2 Adzikhazikitsa mafumu a dziko lapansi,Nacita upo akulu pamodzi,Kutsutsana naye Yehova, ndi Wodzozedwa wace, ndi kuti.
3 Tidule zomangira zao,Titaye nsinga zao.
4 Wokhala m'mwambayo adzaseka;Ambuye adzawanyoza.
5 Pomwepo adzalankhula nao mu mkwiyo wace,Nadzawaopsa m'ukali wace:
6 Koma Ine ndadzoza mfumu yangaPa Ziyoni, phiri langa loyera.
7 Ndidzauza za citsimikizo:Yehova ananena ndiIne, Iwe ndiwe Mwana wanga;Ine lero ndakubala.