5 Pomwepo adzalankhula nao mu mkwiyo wace,Nadzawaopsa m'ukali wace:
6 Koma Ine ndadzoza mfumu yangaPa Ziyoni, phiri langa loyera.
7 Ndidzauza za citsimikizo:Yehova ananena ndiIne, Iwe ndiwe Mwana wanga;Ine lero ndakubala.
8 Undifunse, ndipo ndidzakupatsa amitundu akhale colowa cako,Ndi malekezero a dziko lapansi akhale ako ako.
9 Udzawatyola ndi ndodo yacitsulo;Udzawaphwanya monga mbiya yawoumba.
10 Tsono, mafumu inu, citani mwanzeru:Langikani, oweruza inu a dziko lapansi.
11 Tumikirani Yehova ndi mantha,Ndipo kondwerani ndi cinthenthe.