9 Udzawatyola ndi ndodo yacitsulo;Udzawaphwanya monga mbiya yawoumba.
10 Tsono, mafumu inu, citani mwanzeru:Langikani, oweruza inu a dziko lapansi.
11 Tumikirani Yehova ndi mantha,Ndipo kondwerani ndi cinthenthe.
12 Mpsompsoneni Mwanayo, kuti angakwiye, ndipo mungatayike m'njira,Ukayaka pang'ono pokha mkwiyo wace.Odala onse akumkhulupirira Iye.