1 Yehova, adzasekera mfumu mu mphamvu yanu;Adzakondwera kwakukuru m'cipulumutso canu!
2 Mwampatsa iye cikhumbo ca mtimawace,Ndipo simunakana pempho la milomo yace.
3 Pakuti mumkumika iye ndi madalitso okoma:Muika korona wa golidi woyengetsa pamutu pace.
4 Anakupemphani moyo, mwampatsa iye;Mwamtalikitsira masiku ku nthawi za nthawi.