3 Adzakwera ndani m'phiri la Yehova?Nadzaima m'malo ace oyera ndani?
4 Woyera m'manja, ndi woona m'mtima, ndiye;Iye amene sanakweza moyo wace kutsata zacabe,Ndipo salumbira monyenga,
5 Iye adzalandira dalitso kwa Yehova,Ndi cilungamo kwa Mulungu wa cipulumutso cace.
6 Uwu ndi mbadwo wa iwo akufuna Iye,Iwo akufuna nkhope yanu, Mulungu wa Yakobo.
7 Weramutsani mitu yanu, zipata inu;Ndipo kwezekani inu, zitseko zosatha:Kuti Mfumu ya ulemerero ilowe.
8 Mfumu imene ya ulemerero ndani?Yehova wamphamvu ndi wolimba,Yehova wolimba kunkhondo.
9 Weramutsani mitu yanu, zipata inu;Inde weramutsani, zitseko zosatha inu,Kuti Mfumu ya ulemerero ilowe.