6 Uwu ndi mbadwo wa iwo akufuna Iye,Iwo akufuna nkhope yanu, Mulungu wa Yakobo.
7 Weramutsani mitu yanu, zipata inu;Ndipo kwezekani inu, zitseko zosatha:Kuti Mfumu ya ulemerero ilowe.
8 Mfumu imene ya ulemerero ndani?Yehova wamphamvu ndi wolimba,Yehova wolimba kunkhondo.
9 Weramutsani mitu yanu, zipata inu;Inde weramutsani, zitseko zosatha inu,Kuti Mfumu ya ulemerero ilowe.
10 Mfumu imene ya ulemerero ndani?Yehova wa makamu makamu, Ndiye Mfumu ya ulemerero.