11 Cifukwa ca dzina lanu, Yehova,Ndikhululukireni kusakaza kwanga, pakuti ndiko kwakukuru.
12 Munthuyo wakuopa Yehova ndani?Adzamlangiza iye njira adzasankheyo.
13 Moyo wace udzakhala mokoma;Ndi mbumba zace zidzalandira dziko lapansi.
14 Cinsinsi ca Yehova ciri kwa iwo akumuopa Iye;Ndipo adzawadziwitsa pangano lace.
15 Maso anga alinga kwa Yehova kosaleka;Pakuti Iye adzaonjola mapazi anga m'ukonde.
16 Ceukirani ine ndipo ndicitireni cifundo;Pakuti ndiri woungumma ndi wozunzika.
17 Masautso a mtima wanga akula:Munditurutse m'zondipsinja.