16 Ceukirani ine ndipo ndicitireni cifundo;Pakuti ndiri woungumma ndi wozunzika.
17 Masautso a mtima wanga akula:Munditurutse m'zondipsinja.
18 Penyani mazunzo anga ndi zabvuta zanga;Ndipo khululukirani zolakwa zanga zonse.
19 Penyani adani anga, popeza acuruka;Ndipo andida ndi udani waciwawa.
20 Sungani moyo wanga, ndilanditseni,Ndisakhale nao manyazi, pakuti ndakhulupirira Inu.
21 Ungwiro ndi kuongoka mtima zindisunge,Pakuti ndayembekezera Inu.
22 Ombolani Israyeli, Mulungu, M'masautso ace onse.