19 Penyani adani anga, popeza acuruka;Ndipo andida ndi udani waciwawa.
20 Sungani moyo wanga, ndilanditseni,Ndisakhale nao manyazi, pakuti ndakhulupirira Inu.
21 Ungwiro ndi kuongoka mtima zindisunge,Pakuti ndayembekezera Inu.
22 Ombolani Israyeli, Mulungu, M'masautso ace onse.