1 Mundiweruze, Yehova, pakuti ndayenda m'ungwiro wanga:Ndipo ndakhulupirira Yehova, sindidzaterereka.
2 Mundiyesere, Yehova, ndipo mundisunthe;Yeretsani imso zanga ndi mtima wanga.
3 Pakuti cifundo canu ciri pamaso panga;Ndipo ndayenda m'coona canu.
4 Sindinakhala pansi ndi anthu acabe;Kapena kutsagana nao anthu otyasika.
5 Ndidana nao msonkhano wa ocimwa,Ndipo sindidzakhala nao pansi ocita zoipa.
6 Ndidzasamba manja anga mosalakwa;Kuti ndizungulire guwa la nsembe lanu, Yehova: