4 Sindinakhala pansi ndi anthu acabe;Kapena kutsagana nao anthu otyasika.
5 Ndidana nao msonkhano wa ocimwa,Ndipo sindidzakhala nao pansi ocita zoipa.
6 Ndidzasamba manja anga mosalakwa;Kuti ndizungulire guwa la nsembe lanu, Yehova:
7 Kuti ndimveketse mau a ciyamiko,Ndi kulalikira nchito zanu zonse zozizwa.
8 Yehova, ndikonda cikhalidwe ca nyumba yanu,Ndi malo akukhalamo ulemerero wanu.
9 Musandicotsere mzimu wanga pamodzi ndi olakwa,Kapena moyo wanga pamodzi ndi anthu okhetsa mwazi:
10 Amene m'manja mwao muli mphulupulu,Ndi dzanja lao lamanja ladzala ndi zokometsera mlandu.