6 Ndidzasamba manja anga mosalakwa;Kuti ndizungulire guwa la nsembe lanu, Yehova:
7 Kuti ndimveketse mau a ciyamiko,Ndi kulalikira nchito zanu zonse zozizwa.
8 Yehova, ndikonda cikhalidwe ca nyumba yanu,Ndi malo akukhalamo ulemerero wanu.
9 Musandicotsere mzimu wanga pamodzi ndi olakwa,Kapena moyo wanga pamodzi ndi anthu okhetsa mwazi:
10 Amene m'manja mwao muli mphulupulu,Ndi dzanja lao lamanja ladzala ndi zokometsera mlandu.
11 Koma ine, ndidzayenda m'ungwiro wanga;Mundiombole, ndipo ndicitireni cifundo.
12 Phazi langa liponda pacidikha:M'masonkhano ndidzalemekeza Yehova.