10 Pakuti wandisiya atate wanga ndi amai wanga,Koma Yehova anditola.
11 Mundiphunzitse njira yanu, Yehova,Munditsogolere pa njira yacidikha,Cifukwa ca adani anga,
12 Musandipereke ku cifuniro ca akundisautsa;Cifukwa zinandiukira mboni zonama ndi iwo akupumira zaciwawa.
13 Ndikadapanda kukhulupirira kuti ndikaone ubwino wa YehovaM'dziko la amoyo, ndikadatanil
14 Yembekeza Yehova:Limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako;Inde, yembekeza Yehova.