5 Pakuti sasamala nchito za Yehova,Kapena macitidwe a manja ace,Adzawapasula, osawamanganso.
6 Wodalitsika Yehova,Pakuti adamva mau a kupemba kwanga.
7 Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi cikopa canga;Mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza:Cifukwa cace mtima wanga ukondwera kwakukuru;Ndipo ndidzamyamika nayo Nyimbo yanga.
8 Yehova ndiye mphamvu yao,Inde mphamvu ya cipulumutso ca wodzozedwa wace.
9 Pulumutsani anthu anu, ndi kudalitsa colandira canu:Muwawetenso, ndi kuwanyamula nthawi zonse.