1 Perekani kwa Yehova, inu ana a amphamvu,Perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.
2 Perekani kwa Yehova ulemerero wa dzina lace:Gwadirani Yehova moyera ndi mokometsetsa.
3 Liu la Yehova liri pamadzi;Mulungu wa ulemerero agunda,Ndiye Yehova pa madzi ambiri.
4 Liu la Yehova ndi lamphamvu;Liu la Yehova ndi lalikurukuru.