3 Liu la Yehova liri pamadzi;Mulungu wa ulemerero agunda,Ndiye Yehova pa madzi ambiri.
4 Liu la Yehova ndi lamphamvu;Liu la Yehova ndi lalikurukuru.
5 Liu la Yehova lithyola mitengo yamkungudza;Inde Yehova athyola mikungudza ya ku Lebano.
6 Aitumphitsa monga mwana wa ng'ombe;Lebano ndi Sirio monga msona wa njati.
7 Liu la Yehova ligawa malawi a moto.
8 Liu la Yehova ligwedeza cipululu;Yehova agwedeza cipululu ca Kadese.
9 Liu la Yehova liswetsa nyama zazikazi,Ndipo lipulula nkhalango:Ndipo m'Kacisi mwace zonse ziri m'mwemo zimati, Ulemerero: