5 Ndinagona ine pansi, ndinagona tulo;Ndinauka; pakuti Yehova anandicirikiza.
6 Sindidzaopa unyinji wa anthu akundizinga ine.
7 Ukani Yehova; ndipulumutseni, Mulungu wanga!Pakuti mwapanda adani anga onse patsaya;Mwawatyola mano oipawo.
8 Cipulumutso nca Yehova;Dalitso lanu likhale pa anthu anu.