7 Inu, Yehova, munakhazikitsa phiri langa ndi kuyanja kwanu:Munabisa nkhope yanu; ndinaopa.
8 Ndinapfuulira kwa Inu, Yehova;Kwa Yehova ndinapemba:
9 M'mwazi mwanga muli phindu lanji, potsikira ine kudzenje?Ngati pfumbi lidzayamika Inu? ngati lidzalalikira coonadi canu?
10 Mverani, Yehova, ndipo ndicitireni cifundo:Yehova, mundithandize ndi Inu.
11 Munasanduliza kulira kwanga kukhale kusekera;Munandibvula ciguduli canga, ndipo munandibveka cikondwero:
12 Kuti ulemu wanga uyimbire Inu, wosakhala cete.Yehova Mulungu wanga, ndidzakuyamikani nthawi zonse.