7 Mngelo wa Yehova azinga kuwacinjiriza iwo akuopa Iye,Nawalanditsa iwo.
8 Talawani, ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino;Wodala munthuyo wakukhulupirira Iye.
9 Opani Yehova, inu oyera mtima ace;Cifukwa iwo akumuopa Iye sasowa.
10 Misona ya mkango isowa nimva njala:Koma iwo akufuna Yehova sadzasowa kanthu kabwino.
11 Idzani ananu ndimvereni ine:Ndidzakulangizani zakumuopa Yehova.
12 Munthu wokhumba moyo ndani,Wokonda masiku, kuti aone zabwino?
13 Uletse lilime lako lisachule zoipa,Ndipo milomo yako isalankhule cinyengo.