1 Tsutsanani nao iwo akutsutsana nane, Yehova:Limbanani nao iwo akulimbana nane.
2 Gwirani cikopa cocinjiriza, Ukani kundithandiza.
3 Sololani nthungo, ndipo muwatsekerezere kunjira akundilondola:Nenani ndi moyo wanga, Cipulumutso cako ndine.
4 Athe nzeru nacite manyazi iwo akufuna moyo wanga:Abwezedwe m'mbuyo nasokonezeke iwo akundipangira ciwembu.