18 Ndidzakuyamikanimumsonkhano waukuru:M'cikhamu ca anthu ndidzakulemekezani.
19 Adani anga asandikondwerere ine monyenga;Okwiya nane kopanda cifukwa asanditsinzinire.
20 Pakuti salankhula zamtendere:Koma apangira ciwembu odekha m'dziko.
21 Ndipo andiyasamira m'kamwa mwao;Nati, Hede, Hede, diso lathu lidacipenya.
22 Yehova, mudacipenya; musakhale cete:Ambuye, musakhale kutali ndi ine.
23 Galamukani, ndipo khalani maso kundiweruzira mlandu wanga,Mulungu wanga ndi Ambuye wanga,
24 Mundiweruze monga mwa cilungamo canu, Yehova Mulungu wanga;Ndipo asandisekerere ine.